Anti-Presidential Immunity Initiative Launched

CDEDI together with six other organisations and a number of rights activists and concerned citizens have launched ‘Action Against Presidential Immunity (API)’. The launch took place today at a press conference held in Lilongwe.

The API initiative is intended to compel President Dr. Lazarus Chakwera and his Tonse Alliance administration to own up and deliver campaign promises, especially on scraping off the presidential immunity as a means to ending corruption in Malawi.

Below is the full statement delivered during the press conference

PRESIDENTIAL IMMUNITY MUST FALL; LET’S END POLITICAL IMPUNITY

The Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), in collaboration with the Pan-African Civic Educators Network (PACENET), the Social Revolution Movement (SRM), Centre for Democracy Watch (CEDWAT),CORE Malawi, Mzuzu and Karonga Youth Caucuses, together with a number of individual Human Rights Activists and Concerned Citizens, would like to inform all Malawians that we are championing an initiative called ‘Action Against Presidential Immunity (API)’, aimed at setting a precedent to stop politicians from taking  Malawians for granted and, to ensure that politicians do not get away with their unfulfilled campaign promises and lies.

API, therefore, calls upon all well-meaning Malawians to join hands in forcing President Dr. Lazarus Chakwera and his Tonse Alliance administration to own up and deliver on their sugar-coated campaign promises, which they made prior to the June 23, 2020 court-sanctioned Fresh Presidential Election. One of such flagship promises was to scrape off the presidential immunity as a means to ending corruption in Malawi.

We have taken this position following the expiry of a two-week ultimatum which CDEDI gave President Chakwera on the 4th of July 2022, to direct the Law Commission and the Attorney General to start the process of amending Section 91 of the Constitution, as one way of honouring his pledge of trimming presidential powers.

By scrapping off presidential immunity, Dr. Chakwera would not only have delivered on one of his flagship campaign promises, rather he would have also made a bold statement that he was not entangled in any corruption scandals that have rocked the country in the two years of his leadership, as feared by some quarters.

It is important to remind President Chakwera that he is using borrowed powers, according to Section 12 of the Republican Constitution; therefore, he neither has power to decide the right time to honour his campaign promises nor the luxury to prioritise them.

Our message to President Chakwera is very simple: Scrape off presidential immunity and show Malawians that you are not compromised in any way, especially in leading the fight against corruption, or keep changing tunes and goal posts on your campaign promises, and risk being branded a liar. The latter, however, will make you not fit to serve in the high office of the presidency.

It is against this background that API hereby announces plans to hold nationwide peaceful demonstrations on July 28 2022 to push President Chakwera to scrape off presidential immunity and, also, give a clear direction on how his government will deliver the rest of the promises, complete with a clear time-frame. Detailed information about the demonstrations will be given in due course.

See signatories at the end of Chichewa Statement

———

CHICHEWA

 

Bungwe la CDEDI komanso mabungwe ena asanu ndi limodzi kudzanso anthu ena omenyera ufulu wa anthu ndi mzika zokonda dziko lino, akhazikitsa ntchito yofuna kuthetsa lamulo lomwe limateteza mtsogoleri wadziko kuimbidwa mlandu ngati pafunika kutero.

Pokhazikitsa ntchitoyi pamsonkhano wa atolankhani mumzinda wa Lilongwe, akulu akuluwa ati ntchitoyi yomwe pachingelezi ikutchedwa kuti ‘Action Against Presidential Immunity (API), yatsindika pamfundo yoti mtsogoleri wadzikolino Dr. Lazarus Chakwera ndi Boma lake la Tonse Alliance akwanilitse malonjezo awo apa kampeni oti adzachotsa malamulo omwe amatchinjiriza kuti mtsogoleri wadziko asamazengedwe mulandu kufikila nthawi yaulamuliro wake itatha, ngati njira imodzi yolimbana ndi katangale komanso ziphuphu m’dziko la Malawi.

Werengani zomwe zinawerengedwa pa msonkhanowu

LAMULO LOTCHINJIRIZA KUTI MTSOGOLERI WADZIKO ASAMAZENGEDWE MILANDU KUFIKILA NTHAWI YAULAMULIRO WAKE ITATHA LICHOTSEDWE! MCHITIDWE WOSAKWANIRITSA MALONJEZO PA NDALE UTHE!

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), mogwirizana ndi mabungwe a Pan-African Civic Educators Network (PACENET), Social Revolution Movement (SRM), Centre for Democracy Watch (CEDWAT), CORE Malawi, Mzuzu ndi Karonga Youth Caucuses, komanso gulu la anthu ochuluka omenyera ufulu wachibadwidwe wa anthu, kuphatikizapo Mbadwa zokhudzidwa, akudziwitsa  a Malawi  onse kuti tsopano maguluwa ayamba ntchito yofuna kuti lamulo lotchinjiriza mtsogoleri wa dziko kuti asayimbidwe mlandu lichotsedwe. Mtchitoyi ikudziwika ndi dzina loti – ‘Action Against Presidential Immunity: (API) pachingerezi.

Cholinga cha ntchito imeneyi ndichofuna  kuti atsogoleri andale asamatengere mzika za dziko lino ku mtoso, pomawanamiza ndicholinga choti awavotere pamene anthu andalewo akudziwa ndithu kuti sakwaniritsa malonjezo awo.

Choncho gulu la API, likumema a Malawi onse akufuna kwabwino kuti agwirane manja pokakamiza President Dr. Lazarus Chakwera ndi Boma lake la Tonse Alliance kuti akwanilitse malonjezo awo apa kampeni imene inachitika pa chisankho cha pa June 23, 2020 mmene amakopa anthu khothi litalamula kuti chisankho chichitikenso.

Limodzi mwa malonjezowa linali lakuti adzachotsa malamulo omwe amatchinjiriza kuti mtsogoleri wadziko asamazengedwe mulandu kufikila nthawi yaulamuliro wake itatha, ngati njira imodzi yolimbana ndi katangale komanso ziphuphu m’dziko la Malawi.

Ntchito ya API yayamba chifukwa chakutha kwa nthawi yomwe bungwe la CDEDI linapereka masabata awiri apitawo kwa mtsogoleri wadziko lino Dr. Chakwera kuyambila pa 4th July 2022, kuti alamule bungwe lowona za  malamulo la Law Commission komanso ofesi ya Mulangizi wamkulu wa boma pa nkhani yamalamulo – Attorney General – kuti ayambepo ndondomeko yosintha gawo 91 la malamulo adziko la Malawi ngati njira imodzi yokwanilitsila malonjezo apa kampeni kuti adzachepetsako mphamvu za mtsogoleri wadziko.

Pakuchotsa malamulo okuti mtsogoleri wadziko asamazengedwe mulandu kufikila nthawi yaulamuliro wake itatha, Dr. Chakwera, sangokwanilitsa chabe chimodzi mwa malonjezo apa kampeni, koma zisonyezanso kuti sakukhudzidwa mwanjira ina iliyonse pa nkhani yakatangale ndi ziphuphu yomwe pakadali pano ili kubwalo la milandu.

Ndikofunika kwambiri kuwakumbutsa Dr. Chakwera kuti akugwiritsa ntchito mphamvu zobwereka, malingana ndi gawo 12 la malamulo adziko la Malawi, choncho alibe mphamvu zopanga chiganizo pa iwo wokha chosankha nthawi yabwino yokuti akwanilitsile malonjezo apa kampeni komanso danga lokuti asankhe malonjezo oyenera kuwakwaniritsa koyambirira.

Uthenga wathu kwa a Chakwera siwapatali ayi, ife tikuwalamulo iwo kuti achotse lamulo lotchinjiriza mtsogoleri wadziko kuti asamazengedwe mulandu ndipo izi zisimikidzira kuti Dr. Chakwera ali ndi chidwi ndi ntchito yolimbana ndi katangale mdziko muno. Koma akapitiliza kuchita njomba pa malonjezo ake, maka maka posakwaniritsa malonjezo ake, ndiye kuti anthu ataya chikhulupiliro mwa iye chifukwa cha bodza lomwe lakhala likuonekeratu pakukanika kukwanilitsa malonjezowo. Ndipo zikafika pamenepa ndiye kuti Dr. Chakwera salinso oyenela kukhala mtsogoleri wadziko.

Pachifukwa chimenechi,

API ikulengeza za zionetselo za bata ndi mtendere zomwe zidzachitike pa July 28 2022 pofuna kukakamiza Dr. Chakwera kuti achotse zina mwa mphamvu zake zimene zikumutchinjiriza kuti asamazengedwe mulandu kufikila nthawi yaulamuliro wake itatha, komanso kuti apereke  tsatanetsatane wa ndondomeko yomwe Boma lake layika pofuna kukwanilitsa malonjezo apa kampeni ya mu chaka cha 2020.

Ndondomeko yonse yam’mene zionetselozi zitayendere ifotokozedwa bwino m’masiku akudzawa ndipo a Malawi adziwitsidwa.

Uthengawu walembedwa komanso kuvomerezedwa ndi;

SYLVESTER NAMIWA-CDEDI   0993462700

PHINZIRO MVULA-SRM  0999482170

OLIVE MPINA-PACENET  0995327460

GOMEZGANI NKHOMA-MYC  0884380894

LEVIE LUWEMBA-CEDWAT  0999953041

ATUSAYE SIBALE-KYC  0888439772

STEVE CHIMWAZA-CONCERNED CITIZEN 0992333222

ULEMU MKALO-CONCERNED CITIZEN 0887255570

KELVIN CHIRWA-ACTVIST  0994205333

ZAINAB HASSAN-CONCERNED CITIZEN 0883476757

MUNDANGO NYIRENDA-CONCERNED CITIZEN 0999759653

WELLS KHAMA-CONCERNED CITIZEN 0999368078

RODNY SALAMU-ACTVIST 0991394800

VALENTINO FREDDIE NKHWAZI-CORE MALAWI 0999259393

RICHARD MPHEPO-CONCERNED CITIZEN 0997939404