“Tili ndi nkhawa ndi mantha kuti kodi anthu ndi okonzeka ndi chigamulo cha khoti? Kodi akazagamula, anthu ambali zonse azavomereza?Malawi ndi watonse. Tipemphe a Malawi kuti kukazaperekedwa chigamulo: kaya sichinatiyendere enafe; kaya chayendera enawo; nkhani ndiyokuti ngati m’Malawi, tiyeni tizavomereze mokonda dziko lathu kuti mtendere udzipitilira mdziko muno.Kwaife [Ochita malonda], chiwawa chinachilichonse chimatikhudza chifukwa zikamachitika tsiku limeneli sitimapanga malonda. Tsiku kudutsa osapanga malonda ndiye kuti ndikutipha ndithu. Ndiye, uthenga uwuwu wa mtenderewu, ndiokomera kwambirinso ife. Ngati mtendere ulipo ndiye kuti malonda athu tingathe kumapanga momasuka.Ndi pempho kwa wina aliyense amene ali opanga malonda (Vendor) kuti m’mene timachitira nthawi zonse kukamachitika zionetsero (protests) kuti, tiyeninso patsikuli tisadzatengenawo gawo. Ifenso ngati mavenda tili ndi mbali zosiyiana siyana za zipani zomwe timasapota, koma, tidzachivomereze chigamulo chimenechi mwa mtendere.Tikupempha atsogoleri azipani zimene zikukhudzidwa ndi nkhani imeneyi kuti awakonzekeretse owatsatira awo kuti azavomereze chigamulo chakhoti opanda ziwawa.”
Mark Namponya, Chairperson Lilongwe Urban Association